5 Otsala a akufa sanakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka cikwi. Ndiko kuuka kwa akufa koyamba.
6 Wodala ndi woyera mtima ali iye amene acita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yaciwiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzacita ufumu pamodzi ndi iye zaka cikwizo.
7 Ndipo pamene zidzatha zaka cikwi, adzamasulidwa Satana m'ndende yace;
8 nadzaturuka kudzasokeretsa amitundu ali mu ngondya zinai za dziko, Gogo, ndi Magogo, kudzawasonkhanitsa acite nkhondo: ciwerengero cao ca iwo amene cikhala ngati mcenga wa kunyanja.
9 Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo: ndipo unatsika mota wakumwamba nuwanyeketsa.
10 Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya mota ndi sulfure, kumeneko kulinso ciromboco ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku ku nthawi za nthawi.
11 Ndipo ndinaona, mpando wacifumu waukuru woyera, ndi iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pace, ndipo sanapezedwamalo ao.