1 Ndipo mngelo wacisanu anaomba, ndipo ndinaona nyenyezi yocokera kumwamba idagwa padziko; ndipo anampatsa iye cifunguliro ca dzenje la phompho.
2 Ndipo anatsegula pa dzenje la phompho; ndipo unakwera utsi woturuka m'dzenjemo, ngati utsi wa ng'anjo yaikuru; ndipo dzuwa ndi thambo zinada, cifukwa ca utsiwo wa kudzenje,
3 Ndipo m'utsimo mudaturuka dzombe padziko, ndipo analipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko ziri ndi mphamvu.
4 Ndipo ananena kwa ilo kuti lisaipse udzu wa padziko, kapena cabiriwiri ciri conse, kapena mtengo uli wonse, koma anthu amene alibe cizindikilo ca Mulungu pamphumi pao ndiwo.
5 Ndipo anapatsa ilo mphamvu si kuti likawaphe, komatu kuti likawazunze miyezi isanu; ndipo mazunzidwe ao anali ngati mazunzidwe a cinkhanira, pamene ciluma munthu.