5 Ndipo anapatsa ilo mphamvu si kuti likawaphe, komatu kuti likawazunze miyezi isanu; ndipo mazunzidwe ao anali ngati mazunzidwe a cinkhanira, pamene ciluma munthu.
6 Ndipo m'masiku ajawo, anthu adzafunafuna imfa osaipeza konse; ndipo adzakhumba kumwalira, koma imfa idzawathawa.
7 Ndipo maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukacita nkhondo; ndi pamitu pao ngati akorona onga agolidi, ndi pankhope pao ngati pankhope pa anthu.
8 Ndipo anali nalo tsitsi Ionga tsitsi la akazi, ndipo mano ao analingati mano a mikango.
9 Ndipo anali nazo zikopa ngati zikopa zacitsulo; ndipo mkokomo wa: mapiko ao ngati mkokomo wa agareta, a akavalo ambiri akuthamangira kunkhondo.
10 Ndipo liri nayo micira yofanana ndi ya cinkhanira ndi mbola; ndipo m'micira mwao muli mphamvu yao yakuipsa anthu miyezi isanu.
11 Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa phompho; dzina lace m'Cihebri Abadoni, ndi m'Cihelene ali nalo dzina Apoliyoni.