7 Ndipo maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukacita nkhondo; ndi pamitu pao ngati akorona onga agolidi, ndi pankhope pao ngati pankhope pa anthu.
8 Ndipo anali nalo tsitsi Ionga tsitsi la akazi, ndipo mano ao analingati mano a mikango.
9 Ndipo anali nazo zikopa ngati zikopa zacitsulo; ndipo mkokomo wa: mapiko ao ngati mkokomo wa agareta, a akavalo ambiri akuthamangira kunkhondo.
10 Ndipo liri nayo micira yofanana ndi ya cinkhanira ndi mbola; ndipo m'micira mwao muli mphamvu yao yakuipsa anthu miyezi isanu.
11 Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa phompho; dzina lace m'Cihebri Abadoni, ndi m'Cihelene ali nalo dzina Apoliyoni.
12 Tsoka loyamba lapita; taonani, akudzanso masoka awiri m'tsogolomo.
13 Ndipo mngelo wacisanu ndi cimodzi anaomba, ndipo ndinamva mau ocokera ku nyanga za guwa la nsembe lagolidi liri pamaso pa Mulungu,