29 Koma iyeyo, pakumva, ananyamuka msanga, nadza kwa iye.
30 (Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye)
31 Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Mariya ananyamuka msanga, naturuka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.
32 Pomwepo Mariya, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona iye, anagwa pa mapazi ace, nanena ndi iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.
33 Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, nabvutika mwini,
34 nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi iye, Ambuye, tiyeni, mukaone.
35 Yesu analira.