29 Cifukwa cace Pilato anaturukira kunja kwa iwo, nati, Cifukwa canji mwadza naco ca munthu uyu?
30 Anayankha nati kwa iye, Akadakhala wosacita zoipa uyu sitikadampereka iye kwa inu.
31 Ndipo Pilato anati kwa iwo, Mumtenge iye inu, ndi kumweruza iye monga mwa cilamulo canu. Ayuda anati kwa iye, Tiribe ulamuliro wakupha munthu ali yense;
32 kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene, akuti adzafa nayo.
33 Cifukwa cace Pilato analowanso m'Pretorio, naitana Yesu, nati kwa iye, Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda kodi?
34 Yesu anayankha, Kodi munena ici mwa inu nokha, kapena ena anakuuzani za Ine?
35 Pilato anayankha, ndiri ine Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe akulu anakupereka kwa ine; wacita ciani?