1 Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa akuphunzira ace ku nyanja ya Tiberiya. Koma anadzionetsera cotere.
2 Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wochedwa Didimo, ndi Natanayeli wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedayo, ndi awiri ena a akuphunzira ace.
3 Simoni Petro ananena nao, ndinka kukasodza. Ananena naye, Ifenso tipita nawe. Anaturuka, nalowa m'ngalawa; ndipo m'usiku muja sanagwira kanthu.
4 Koma pakuyamba kuca, Yesu anaimirira pam bali pa nyanja, komatu akuphunzirawo sanadziwa kuti ndiye Yesu.
5 Yesu ananena nao, Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi? Anamyankha iye, lai.
6 Koma anati kwa iwo, Ponyani khoka ku mbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza, Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka cifukwa ca kucuruka nsomba.
7 Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadzibveka maraya a pathupi, pakuti anali wamarisece, nadziponya yekha m'nyanja.