1 Koma panali munthu wa Afarisi, dzina lace Nikodemo, mkulu wa Ayuda,
2 Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wocokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kucita zizindikilo zimene inu mucita, ngati Mulungu sakhala naye,
3 Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.
4 Nikodemoananena kwa iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amace ndi kubadwa?
5 Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.