18 Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupira waweruzidwa ngakhale tsopano, cifukwa sanakhulupirira dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.
19 Koma ciweruziro ndi ici, kuti kuunika kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti nchito zao zinali zoipa.
20 Pakuti yense wakucita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe nchito zace.
21 Koma wocita coonadi adza kukuunika, kuti nchito zace zionekere kuti zinacitidwa mwa Mulungu.
22 Zitapita in anadza Yesu ndi akuphunzira ace ku dziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza.
23 Ndipo Yohane analinkubatiza m'Ainoni pafupi pa Salemu, cifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.
24 Pakuti Yohane sanaikidwe m'ndende.