6 Cobadwa m'thupi cikhala thupi, ndipo cobadwa mwa Mzimu, cikhala mzimu.
7 Usadabwe cifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano.
8 Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ace, komavsudziwa, kumene icokera, ndi kumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu.
9 Nikodemo anayankha nati kwa iye, Izi zingatheke bwanji?
10 Yesu anayankha nati kwa iye, Kodi uli mphunzitsi wa Israyeli, ndipo sudziwa izi?
11 Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula cimene ticidziwa, ndipo ticita umboni za cimene taeiona; ndipo umboni wathu simuulandira.
12 Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupira, mudzakhulupira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba?