18 Ndipo mfumu inapanga mpando waukulu wacifumu waminyanga, naukuta ndi golidi woyengetsa.
19 Mpandowo wacifumu unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndi pamwamba pa mpando wacifumu panali pozungulira kumbuyoko, ndipo munali ngati manja m'mbali zonse ziwiri za pokhalirapo, naimika mikango iwiri m'mbali mwa manjawo.
20 Ndipo anaimikamikango khumi ndi iwiri mbali yina ndi yina, pa makwerero asanu ndi limodzi aja; m'dziko liri lonse tina simunapangidwa wotere.
21 Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomo zinali zagolidi, ndi zotengera zonse za nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano zinali zagolidi yekha yekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva ana ngoyesedwa opanda pace masiku onse a Solomo.
22 Popeza mfumu inali nazo panyanja zombo za ku Tarisi, pamodzi ndi zombo za Hiramu; zombo za ku Tarisi zinafika, kamodzi zitapita zaka zitatu, ziri nazo golidi, ndi siliva, ndi minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za maanga maanga.
23 Ndipo mfumu Solomo anawaposa mafumu onse a dziko lapansi pa cuma ndi nzeru.
24 Ndipo anthu onse a pa dziko anafuna nkhope ya Solomo, kudzamva nzeru zace zimene Mulungu analonga m'mtima mwace.