21 Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomo zinali zagolidi, ndi zotengera zonse za nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano zinali zagolidi yekha yekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva ana ngoyesedwa opanda pace masiku onse a Solomo.
22 Popeza mfumu inali nazo panyanja zombo za ku Tarisi, pamodzi ndi zombo za Hiramu; zombo za ku Tarisi zinafika, kamodzi zitapita zaka zitatu, ziri nazo golidi, ndi siliva, ndi minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za maanga maanga.
23 Ndipo mfumu Solomo anawaposa mafumu onse a dziko lapansi pa cuma ndi nzeru.
24 Ndipo anthu onse a pa dziko anafuna nkhope ya Solomo, kudzamva nzeru zace zimene Mulungu analonga m'mtima mwace.
25 Ndipo akafika munthu yense ndi mtulo wace, zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolidi, ndi zobvala, ndi zida, ndi zonunkhira, ndi akavalo, ndi nyuru; momwemo caka ndi caka.
26 Ndipo Solomo anasonkhanitsa, magareta ndi apakavalo; anali nao magareta cikwi cimodzi mphambu, mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri, nawasungira m'midzi yosungamo magareta, ndi kwamfumu m'Yerusalemu.
27 Ndipo mfumu inacurukitsa siliva ngati miyala m'Yerusalemu, ndi mitengo yamikungudza anailinganiza ndi mikuyu ya m'madambo.