22 Ndipo mau a Mulungu anafika kwa Semaya mneneri wa Mulungu, nati,
23 Lankhula kwa Rehabiamu mwana wa Solomo mfumu ya Yuda, ndi kwa nyumba yonse ya Yuda, ndi Benjamini, ndi kwa anthu otsalawo, nuti,
24 Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israyeli, bwererani yense kunyumba kwace; popeza cinthuci cacokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.
25 Ndipo Yerobiamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efraimu, nakhalamo, naturukamo, namanga Penueli.
26 Ndipo Yerobiamu ananena m'mtima mwace, Ufumuwu udzabwereranso ku nyumba ya Davide.
27 Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m'nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda.
28 Potero mfumu inakhala upo, napanga ana a ng'ombe awiri agolidi, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisrayeli inu milungu yanu imene inakuturutsani m'dziko la Aigupto.