25 Ndipo Yerobiamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efraimu, nakhalamo, naturukamo, namanga Penueli.
26 Ndipo Yerobiamu ananena m'mtima mwace, Ufumuwu udzabwereranso ku nyumba ya Davide.
27 Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m'nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda.
28 Potero mfumu inakhala upo, napanga ana a ng'ombe awiri agolidi, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisrayeli inu milungu yanu imene inakuturutsani m'dziko la Aigupto.
29 Ndipo anaimika mmodzi ku Beteli, naimika wina ku Dani.
30 Koma cinthu ici cinasanduka: chimo, ndipo anthu anamka ku mmodziyo wa ku Dani.
31 Iye namanga nyumba za m'misanje, nalonga anthu acabe akhale ansembe, osati ana a Levi ai.