8 Koma iye analeka uphungu wa mandodawo, umene anampangirawo, nakafunsira kwa acinyamata anzace oimirira pamaso pace,
9 nati kwa lwo, Kodi inu mundipangire bwanji kuti tiyankhe anthu awa anandiuza ine, kuti, Mupepuze gori limene atate wanu anatisenza ife?
10 Ndipo acinyamata anzace ananena naye, Dati, Mzitero ndi anthu awa adalankhula nanu, nati, Atate wanu analemeretsa gori lathu, koma inu mutipepuzire limenelo; mzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'cuuno mwa atate wanga.
11 Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzani gori lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa gori lanu, atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
12 Ndipo Yerobiamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehabiamu tsiku lacitatu monga momwe anawauzira mfumu, nati, Bweraninso kwa ine tsiku lacitatu.
13 Ndipo mfumu inayankha anthu mau okalipa, naleka uphungu anampangira mandodawo,
14 nalankhula nao monga mwa uphungu wa acinyamata, nati, Atate wanga analemeretsa gori lanu, koma ine ndidzaonjezerapo pa gori lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira,