7 Ndipo macitidwe ace ena a Abiya, ndi zonse anazicita, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobiamu.
8 Nagona Abiya ndi makolo ace, namuika anthu m'mudzi wa Davide; Asa mwana wace nalowa ufumu m'malo mwace.
9 Ndipo caka ca makumi awiri ca Yerobiamu mfumu ya Israyeli, Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda.
10 Nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai mphambu cimodzi, ndipo dzina la amace linali Maaka mwana wa Abisalomu.
11 Ndipo Asa anacita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lace.
12 Nacotsa m'dziko anyamata aja adama, nacotsanso mafano onse anawapanga atate ace.
13 Ndipo anamcotsera Maaka amace ulemu wa mace wa mfumu, popeza iye anapanga fano lonyansitsa likhale cifanizo; ndipo Asa analikha fano lace, nalitentha ku mtsinje wa Kidroni.