1 Mafumu 2:3-9 BL92

3 nusunge cilangizo ca Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zace, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wace, monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose, kuti ukacite mwa nzeru m'zonse ukacitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako;

4 kuti Yehova akakhazikitse mau ace adanenawo za ine, kuti, Ngati ana ako akasunga bwino njira zao, kuyenda moona pamaso pa Ine ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, nditi sipadzakusowa mwamuna mmodzi pa mpando wacifumu wa Israyeli.

5 Ndiponso udziwa cimene Yoabu mwana wa Zeruya anandicitira, inde cimene anawacitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israyeli, ndiwo Abineri mwana wa Neri, ndi Amasa mwana wa Yeteri, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lace la m'cuuno mwace, ndi pa nsapato za pa mapazi ace.

6 Cita mwa nzeru yako tsono, osalola mutu wace waimvi utsikire kumanda ndi mtendere.

7 Koma ucitire zokoma ana amuna aja a Barizilai wa ku Gileadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.

8 Ndipo taona uli naye Simeyi mwana wa Gera wa pfuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikuru tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordano, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga,

9 Ndipo tsono, usamuyesera iye wosacimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumcitira iye, nutsitsire mutu wace waimvi ndi mwazi kumanda.