3 Ndipo mfumu ya Israyeli ananena ndi anyamata ace, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Gileadi ngwathu, ndipo tangokhala cete, osaulanditsa m'dzanja la mfumu ya Aramu.
4 Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Gileadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israyeli, M'mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavale ako.
5 Ndipo Yehosafati ananena ndi mfumu ya Israyeli, Fuusira ku mau a Yehova lero.
6 Pamenepo mfumu ya Israyeli inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Gileadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu.
7 Koma Yehosafati anati, Kodi pano palibe mneneri wina wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?
8 Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wace wa Yimla. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.
9 Tsono mfumu ya Israyeli anaitana mdindo, nati, Kamtenge msanga Mikaya mwana wa Yimla.