21 Ndipo Solomo analamulira maiko onse, kuyambira ku Firate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Aigupto; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomo masiku onse a moyo wace.
22 Ndipo zakudya za Solomo zofikira tsiku limodzi zinalr miyeso makumi atatu ya ufa wosalala, ndi miyeso makumi asanu ndi limodzi ya ufa wamankhupete,
23 ng'ombe zonenepa khumi, ndi ng'ombe za kubusa makumi awiri, ndi nkhosa zana limodzi, osawerenganso ngondo ndi nswala ndi mphoyo ndi mbalame zoweta.
24 Pakuti analamulira dziko lonse liri tsidya lino la Firate, kuyambira ku Tipsa kufikira ku Gaza, inde mafumu onse a ku tsidya tino la Firate; nakhala ndi mtendere kozungulira konseko,
25 Ndipo Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wace ndi mkuyu wace, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.
26 Ndipo Solomo anali nazo zipinda za akavalo a magareta ace zikwi makumi anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri.
27 Ndipo akapitao aja anatengetsera cakudya Solomo ndi anthu onse akudya ku gome la mfumu Solomo, munthu yense m'mwezi mwace, sanalola kanthu kasoweke.