13 Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo inu nthawi zosatha.
14 Ndipo mfumu inapotoloka nkhope yace, nidalitsa msonkhano wonse wa Israyeli, Ndi msonkhano wonse wa Israyeli unaimirira.
15 Nati iye, Wolemekezeka ndi Yehova Mulungu wa Israyeli amene analankhula m'kamwa mwace ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi dzanja lace, nati,
16 Kuyambira tsiku lakuturutsa Ine anthu anga Aisrayeli m'dziko la Aigupto, sindinasankha mudzi uli wonse mwa mafuko onse a Israyeli kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, koma ndinasankha Davide kukhala mfumu ya anthu anga Aisrayeli.
17 Ndipo Davide atate wanga anafuna m'mtima mwace kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.
18 Koma Yehova ananena ndi Davide atate wanga, Popeza unafuna m'mtima mwako kumangira dzina langa nyumba, unacita bwino kuti m'mtima mwako unatero.
19 Koma usamange ndiwe nyumbayo, koma mwana wako adzaturuka m'cuuno mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumba.