1 Ndipo kunali, atatsiriza Solomo kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi cifuniro conse ca Solomo anacikhumbaco,
2 Yehova anaonekera kwa Solomo nthawi yaciwiri, monga momwe adamuonekera ku Gibeoni.
3 Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.
4 Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga, monga momwe Davide atate wako anayendera ndi mtima woona ndi wolungama, kuzicita zonse ndakulamulirazo, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga,
5 pamenepo Ine ndidzakhazikitsa cimpando ca ufumu wako pa Israyeli nthawi yosatha, monga ndinalonjezana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wamwamuna pa mpando wacifumu wa Israyeli.