16 Pakuti Farao mfumu ya Aigupto adakwera nalanda Gezeri, nautentha ndi moto, nawapha Akanani akukhala m'mudzimo, naupereka kwaulere kwa mwana wace mkazi wa Solomo.
17 Ndipo Solomo anamanganso Gezeri, ndi Betihoroni wakunsi,
18 ndi Balati, ndi Tadimori wa m'cipululu m'dziko muja,
19 ndi midzi yonse yosungamo zinthu zace za Solomo, ndi midzi yosungamo magareta ace, ndi midzi yokhalamo apakavalo ace, ndi zina ziti zonse zidakomera Solomo kuzimanga m'Yerusalemu, ndi ku Lebano, ndi m'dziko lonse la ufumu wace.
20 Ndipo Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi otsala, amene sanali a ana a Israyeli,
21 ana ao amene adatsala m'dziko, amene ana a lsrayeli sanakhoza kuononga konse, Solomo anawasenzetsa msonkho wa nchito kufikira lero.
22 Koma Solomo sanawayesa ana a Israyeli akapolo, koma iwowo anali anthu a nkhondo, ndi anyamata ace, ndi akalonga ace, ndi akazembe ace, ndi oyang'anira magareta ace ndi apakavalo ace.