3 Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.
4 Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga, monga momwe Davide atate wako anayendera ndi mtima woona ndi wolungama, kuzicita zonse ndakulamulirazo, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga,
5 pamenepo Ine ndidzakhazikitsa cimpando ca ufumu wako pa Israyeli nthawi yosatha, monga ndinalonjezana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wamwamuna pa mpando wacifumu wa Israyeli.
6 Koma mukadzabwerera pang'ono pokha osanditsata, kapena inu, kapena ana anu, osasunga malamulo anga ndi malemba anga amene ndawaika pamaso panu; mukadzatumikira milungu yina ndi kuilambira;
7 pamenepo Ine ndidzalikha Aisrayeli kuwacotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba yino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israyeli adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.
8 Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali yino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero cifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba yino?
9 Ndipo anthu adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wao amene adaturutsa makolo ao m'dziko la Aigupto, natsata milungu yina, nailambira, naitumikira; cifukwa cace Yehova anawagwetsera coipa conseci.