20 Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zobvala; nafika ku nyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika ku nyumba yace; ndipo powauza anamuikira cakudya, nadya iye.
21 Pamenepo anyamata ace ananena naye, Ici mwacita nciani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya,
22 Nati iye, Pamene mwanayo akali ndi moyo, ndinasala kudya ndi kulira, pakuti ndinati, Adziwa ndani kapena Yehova adzandicitira cifundo kuti mwanayo akhale ndi moyo.
23 Koma tsopano wafa, ndidzasaliranjinso kudya? Kodi ndikhoza kumbweza? Ine ndidzamuka kuli iye, koma iye sadzabweranso kwa ine.
24 Ndipo Davide anasangalatsa Bateseba mkazi wace, nalowa kwa iye, nagona naye; ndipo anabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Solomo. Ndipo Yehova anamkonda iye,
25 natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namucha dzina lace Wokondedwa ndi Yehova, cifukwa ca Yehova.
26 Ndipo Yoabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mudzi wacifumu.