29 Ndipo anyamata a Abisalomu anamcitira Amnoni monga umo Abisalomu anawalamulira. Pomwepo ana amuna onse a mfumu ananyamuka, nakwera munthu yense pa nyuru yace, nathawa.
30 Ndipo kunali akali panjira, mau anafika kwa Davide, kuti, Abisalomu anapha ana amuna onse a mfumu, osatsalapo ndi mmodzi yense.
31 Pamenepo mfumu inanyamuka ning'amba zobvala zace nigona pansi, ndipo anyamata ace onse anaimirirapo ndi zobvala zao zong'ambika.
32 Ndipo Jonadabu mwana wa Simeya mbale wa Davide anayankha nati, Mbuye wanga asaganize kuti anapha anyamata onse, ana amuna a mfumu, pakuti Amnoni yekha wafa, pakuti Ici cinatsimikizika ndi mau a Abisalomu kuyambira tsiku lija anacepetsa mlongo: wace Tamara.
33 Cifukwa cace tsono mfumu mbuye wanga asasauke mtima ndi cinthuci, ndi kuganiza kuti ana amuna onse a mfumu afa; pakuti Amnoni yekha wafa.
34 Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ace nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwace anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.
35 Ndipo Jonadabu ananena ndi mfumu, Onani, ana amuna a mfumu afika; monga ananena mnyamata wanu, momwemo.