25 Pamenepo mlondayo anapfuula, nauza mfumu. Mfumuyo niti, Ngati ali yekha alikubwera ndi mau. Ndipo iye uja anayenda msanga, nayandikira.
26 Ndipo mlondayo anaona munthu wina wothamanga; mlonda naitana wakucipata nanena, Taona munthu wina wakuthamanga yekha. Ndipo mfumu inati, iyenso abwera ndi mau.
27 Mlondayo nati, Ndiyesa kuti kuthamanga kwa wapatsogoloyo kunga kuthamanga kwa Ahimaazi mwana wa Zadoki, Ndipo mfumu inati, iye ndiye munthu wabwino, alikubwera ndi mau okoma.
28 Ndipo Ahimaazi anapfuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yace pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.
29 Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yoabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringu piringu, koma sindinadziwa ngati kutani.
30 Ndipo mfumu inati, Pambuka nuime apa. Napambuka, naimapo.
31 Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera cilango lero onse akuukira inu.