1 Ndipo m'tsogolo mwace Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa; Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.
2 Ndipo anakantha Amoabu nawayesa ndi cingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi cingwe cimodzi cathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amoabu anakhala anthu a Davide, nabwera: nayo mitulo.
3 Davide anakanthanso Hadadezeri, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wace ku cimtsinje ca Firate.
4 Ndipo Davide anatenga apakavalo ace cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi maku mi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magareta, koma anasunga a iwo akufikira magareta zana limodzi.
5 Ndipo pakufika Aaramu a ku Damasiko kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya ku Zoba, Davide anakanthako Aaramu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.
6 Pamenepo Davide anaika maboma m'Aramu wa Damasiko, Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kuli konse anamukako.