3 Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Sauli kuti ndimuonetsere cifundo ca Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Jonatani wopunduka mapazi ace.
4 Ndipo mfumu inanena naye, Ali kuti iyeyo? Ziba nanena kwa mfumu, Onani ali m'nyumba ya Makiri, mwana vya Amiyeli ku Lodebara.
5 Pamenepo Davide anatumiza anthu nakatenga iye ku nyumba ya Makiri mwana wa Amiyeli ku Lodebara.
6 Ndipo Mefiboseti mwana wa Jonatani, mwana wa Sauli, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yace pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu.
7 Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakucitira kukoma mtima cifukwa ca Jonatani atate wako; ndi minda yonse ya Sauli ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa cikhalire.
8 Ndipo iye anamlambira, nati, Mnyamata wanu ndani, kuti mulikupenya garu wakufa monga ine.
9 Pomwepo mfumu inaitana Ziba, mnyamata wa Sauli, ninena naye, Za Sauli zonse ndi za nyumba yace yonse ndampatsa mwana wa mbuye wako.