5 Tsidya lija la Yordano, m'dziko la Moabu, Mose anayamba kufotokozera cilamulo ici, ndi kuti.
6 Yehova Mulungu wathu ananena ndi ife m'Horebe, ndi kuti, Yakwanira nthawi yokhala inu m'phiri muno;
7 bwererani, yendani ulendo wanu ndi kumuka ku mapiri a Aamori, ndi koyandikizana nao, kucidikha, kumapiri, ndi kunsi ndi kumwela, ndi kumphepete kwa nyanja, dziko la Akanani, ndi Lebano, kufikira nyanja yaikuru Firate.
8 Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao.
9 Ndipo muja ndinanena ndi inu, ndi kuti, Sinditha ine kukunyamulani ndekha;
10 Yehova Mulungu wanu anakucurukitsani, ndipo taonani, lero mucuruka ngati nyenyezi za kumwamba.
11 Yehova Mulungu wa makolo anu, acurukitsire ciwerengero canu calero ndi cikwi cimodzi, nakudalitseni monga iye ananena nanu!