9 koma muzimupha ndithu; liyambe dzanja lanu kukhala pa iye kumupha, ndi pamenepo dzanja la anthu onse.
10 Nimuzimponya miyala, kuti afe; popeza anayesa kukucetani muleke Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba va akapolo.
11 Kuti Israyeli wonse amve, ndi kuopa, ndi kusaonieza kucita coipa cotere conga ici pakati pa inu.
12 Ukamva za umodzi wa midzi yanu, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani kukhalako, ndi kuti,
13 Amuna ena opanda pace anaturuka pakati pa inu, naceta okhala m'mudzi mwao, ndi kuti, Timuke titumikire milungu yina, imene simunaidziwa;
14 pamenepo muzifunsira, ndi kulondola, ndi kufunsitsa; ndipo taonani, cikakhala coona, catsimikizika cinthuci, kuti conyansa cotere cacitika pakati pa inu;
15 muzikanthatu okhala m'mudzi muja ndi lupanga lakuthwa; ndi kuuononga konse, ndi zonse ziri m'mwemo, ng'ombe zace zomwe, ndi lupanga lakuthwa.