4 popeza sanakukumikani ndi mkate ndi madzi m'njira muja munaturuka m'Aigupto; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesapotamiya, kuti akutemberereni.
5 Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafuna kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.
6 Musawafunira mtendere, kapena cowakomera masiku anu onse ku nthawi zonse.
7 Musamanyansidwa naye M-edomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye M-aigupto, popeza munali alendo m'dziko lace.
8 Ana obadwa nao a mbadwo wacitatu alowe m'msonkhano wa Yehova.
9 Nkhondo yanu ikaturuka pa adani anu, mudzisunge kusacita coipa ciri conse.
10 Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera cifukwa cocitika usiku, azituruka kunja kwa cigono, asalowe pakati pa cigono;