13 Ndipo munene pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Ndacotsa zopatulika m'nyumba mwanga, ndi kuzipereka kwa Mlevi, ndi kwa mlendo, ndi kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, monga mwa lamulo lanu lonse munandilamulira ine; sindinalakwira malamulo anu, kapena kuwaiwala.