4 Ndipo wansembe alandire mtanga m'manja mwanu, ndi kuuika pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu.
5 Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye M-aramu wakuti atayike, natsika kumka ku Aigupto, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukuru, wamphamvu, ndi wocuruka anthu ace;
6 koma Aaigupto anaticitira coipa, natizunza, natisenza nchito yolimba.
7 Pamenepo tinapfuulira kwa Yehova, Mulungu wa makolo athu; ndipo Yehova anamva mau athu, napenya kuzunzika kwathu, ndi nchito yathu yolemetsa, ndi kupsinjika kwathu;
8 ndipo Yehova anatiturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi kuopsa kwakukuru, ndi zizindikilo, ndi zodabwiza;
9 ndipo anabwera nafe kumalo kuno, natipatsa dziko ili ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.
10 Ndipo tsopano, taonani, ndabwera nazo zoyamba za zipatso za nthaka, zimene Inu, Yehova, mwandipatsa. Ndipo muziike pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kugwadira Yehova Mulungu wanu;