10 Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi adzaona kuti akuchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.
11 Ndipo Yehova adzakucurukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo,
12 Yehova adzakutsegulirani cuma cace cokoma, ndico thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yace, ndi kudalitsa nchito zonae za dzanja lanu; ndipo mudza kongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.
13 Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mcira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwacita;
14 osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu yina kuitumikira.
15 Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kucita malamulo ace onse ndi malemba ace amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani,
16 Mudzakhala otembereredwa m'mudzi, ndi otembereredwa pabwalo.