7 Ndipo pamene munafika pamalo pano, Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basana, anaturuka kudzakomana nafe kunkhondo, ndipo tinawakantha;
8 ndipo tinalanda dziko lao, ndi kulipereka likhale colowa cao ca Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la hafu la Manase.
9 Cifukwa cace sungani mau a cipangano ici ndi kuwacita, kuti mucite mwanzeru m'zonse muzicita.
10 Muimirira inu nonse lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wanu; mafumu anu, mapfuko anu, akuru anu, ndi akapitao anu, amuna onse a Israyeli;
11 makanda anu, akazi anu, ndi mlendo wanu wakukhala pakati pa zigono zanu, kuyambira wotema nkhuni kufikira wotunga madzi;
12 kuti mulowe cipangano ca Yehova Mulungu wanu, ndi lumbiriro lace, limene Yehova Mulungu wanu acita ndi inu lero lino;
13 kuti adzikhazikire inu, mtundu wace wa anthu lero lino, ndi kuti akhale kwa inu Mulungu, monga ananena ndi inu, ndi monga analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo.