4 Otayika anu akakhala ku malekezero a thambo, Yehova Mulungu wanu adzakumemezani kumeneko, nadzakutenganiko;
5 ndipo Yehova Mulungu wanu adzakulowetsani m'dziko lidakhala lao lao la makolo anu, nilidzakhala lanu lanu; ndipo adzakucitirani zokoma, ndi kukucurukitsani koposa makolo anu.
6 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.
7 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaika matemberero awa onse pa adani anu, ndi iwo akukwiya ndi inu, amene anakulondolani.
8 Pamenepo mutembenuke ndi kumvera mau a Yehova, ndi kucita malamulo ace onse amene ndikuuzani lero lino.
9 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakucurukitsirani nchito zonse za dzanja lanu, zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za zoweta zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zikukomereni; popeza Yehova Mulungu wanu adzakondweranso kukucitirani zokoma; monga anakondwera ndi makolo anu;
10 ngati mudzamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kuwasunga malamulo ace ndi malemba ace olembedwa m'buku la cilamulo ici; ngati mudzabwerera kudza kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.