9 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakucurukitsirani nchito zonse za dzanja lanu, zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za zoweta zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zikukomereni; popeza Yehova Mulungu wanu adzakondweranso kukucitirani zokoma; monga anakondwera ndi makolo anu;
10 ngati mudzamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kuwasunga malamulo ace ndi malemba ace olembedwa m'buku la cilamulo ici; ngati mudzabwerera kudza kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.
11 Pakuti lamulo ili ndikuuzani lero lino, silikulakani kulizindikira, kapena silikhala kutali.
12 Silikhala m'mwamba, kuti mukati, Adzatikwerera m'mwamba ndani, ndi kubwera nalo kwa ife, ndi kutimvetsa ili, kuti tilicite?
13 Ndipo silikhala tsidya la nyanja, kuti mukati, Adzatiolokera ndani tsidya la nyanja, ndi kutitengera ili, ndi kutimvetsa ili, kuti tilicite?
14 Pakuti mauwa ali pafupifupi ndi inu, m'kamwa mwanu, ndi m'mtima mwanu, kuwacita.
15 Tapenyani, ndaika pamaso panu lero lino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa;