33 Vinyo wao ndiwo ululu wa zinjoka,Ndi ululu waukali wa mphiri.
34 Kodi sicisungika ndi Ine,Colembedwa cizindikilo mwa cuma canga ceni ceni?
35 Kubwezera cilango nkwanga, kubwezera komwe,Pa nyengo ya kuterereka phazi lao;Pakuti tsiku la tsoka lao layandika,Ndi zinthu zowakonzeratu zifulomira kudza.
36 Popeza Yehova adzaweruza anthuace,Nadzacitira nsoni anthu ace;Pakuona iye kuti mphamvu yao yatha,Wosatsala womangika kapena waufulu,
37 Pamenepo adzati, Iri kuti milunguyao,Thanthwe limene anathawirako?
38 Imene inadya mafuta a nsembe zao zophera,Nimwa vinyo wa nsembe yao yothira?Iuke nikuthandizeni, Ikhale pobisalapo panu.
39 Tapenyani tsopano kuti Ine ndine iye,Ndipo palibe mulungu koma Ine;Ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi mayo:Ndikantha, ndicizanso Ine;Ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.