15 Ndi zinthu zoposa za mapiri akale,Ndi zinthu zofunikatu za zitunda zosatha,
16 Ndi zinthu zofunikatu za dziko lapansi, ndi kudzala kwace,Ndi cibvomerezo ca iye anakhala m'citsambayo;Mdalitso ufike pa mutu wa Yosefe,Ndi pakati pa mutu wace wa iye wokhala padera ndi abale ace.
17 Woyamba kubadwa wa ng'ombe yace, ulemerero ndi wace;Nyanga zace ndizo nyanga zanjati;Adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi.Iwo ndiwo zikwi khumi za Efraimu,Iwo ndiwo zikwi za Manase.
18 Ndi za Zebuloni anati,Kondwera, Zebuloni, ndi kuturukakwako;Ndi Isakara, m'mahema mwako.
19 Adzaitana mitundu ya anthu afike kuphiri;Apo adzaphera nsembe za cilungamo;Popeza adzayamwa zocuruka za m'nyanja,Ndi cuma cobisika mumcenga.
20 Ndi za Gadi anati,Wodala iye amene akuza Gadi;Akhala ngati mkango waukazi,Namwetula dzanja, ndi pakati pa mutu pomwe.
21 Ndipo anadzisankhira gawo loyamba,Popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira;Ndipo anadza ndi mafumu a anthu,Anacita cilungamo ca Yehova,Ndi maweruzo ace ndi Israyeli.