1 Ndipo Mose anakwera kucokera ku zidikha za Moabu, kumka ku phiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Gileadi, kufikira ku Dani;
2 ndi Nafitali lonse, ndi dziko la Efraimu, ndi Manase, ndi dziko lonse la Yuda, kufikira nyanja ya m'tsogolo;
3 ndi kumwela, ndi cidikha eli cigwa ca Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kufikira ku Zoari.
4 Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako.
5 Ndipo Mose mtumiki wa Yehova anamwalirako m'dziko la Moabu, monga mwa mau a Yehova.
6 Ndipo iye anamuika m'cigwa m'dziko la Moabu popenyana ndi Beti-peori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwace kufikira lero lino.
7 Ndipo zaka zace za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lace silinacita mdima, ndi mphamvu yace siidaleka.