1 Ndipo Mose anaitana Israyeli wonse, nanena nao, Tamverani, Israyeli, malemba ndi maweruzo ndinenawa m'makutu mwanu lero, kuti muwaphunzire, ndi kusamalira kuwacita.
2 Yehova Mulungu wathu anapangana nafe cipangano m'Horebe.
3 Yehova sanacita cipangano ici ndi makolo athu, koma ndi ife, ife amene tiri ndi moyo tonsefe pane lero.
4 Yehova ananena ndi inu popenyana maso m'phirimo, ali pakati pa moto,