15 Ndipo uzikumbukilakuti unali kapolo m'dziko la Aigupto, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakuturutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; cifukwa cace Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.
16 Lemekeza atate wako ndi amako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako acuruke, ndi kuti cikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
17 Usaphe.
18 Usacite cigololo.
19 Usabe.
20 Usamnamizire mnzako.
21 Usasirire mkazi wace wa mnzako; usakhumbe nyumba yace ya mnzako, munda wace, kapena wanchito wace wamwamuna, kapena wanchito wace wamkazi, ng'ombe yace, kapena buru wace, kapena kanthu kali konse ka mnzako.