26 Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife, nakhala ndi moyo?
27 Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzicita.
28 Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, pamene munanena ndi ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Ndidamva mau a kunena kwao kwa anthu awa, amene ananena ndi iwe; cokoma cokha cokha adanenaci.
29 Ha! mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti ciwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!
30 Muka, nuti nao, Bwererani ku mahema anu.
31 Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malemba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awacite m'dziko limene ndiwapatsa likhale lao lao.
32 Potero muzisamalira kucita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; musamapatuka kulamanzere kapena kulamanja.