6 Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakuturutsa m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo.
7 Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha.
8 Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciri conse ca zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko;
9 usazipembedzere izo, usazitumikire izo; cifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndine Mulungu wansanje, wakulanga ana cifukwa ca atate wao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
10 ndi kucitira cifundo anthu zikwi, a iwo amene akondana ndi Ine nasunga malamulo anga.
11 Usaehuledzinala Yehova Mulungu wako pacabe; cifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosacimwa amene achula pacabe dzina lacelo.
12 Samalira tsiku la Sabata likhale lopatulika, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira.