11 ndi nyumba zodzala nazo zokoma ziri zonse, zimene simunazidzaza, ndi zitsime zosema, zimene simunazisema, minda yampesa, ndi minda yaazitona, zimene simunazioka, ndipo mutakadya ndi kukhuta;
12 pamenepo mudzicenjere mungaiwale Yehova, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo,
13 Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzichula dzina lace.
14 Musamatsata milungu yina, milungu yina ya mitundu ya anthu akuzinga inu;
15 pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukucotsani pankhope pa dziko lapansi.
16 Musamayesa Yehova Mulungu wanu, monga munamyesa m'Masa.
17 Muzisunga mwacangu malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi mboni zace, ndi malemba ace, amene anakulamulirani.