4 Imvani, Israyeli; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi;
5 ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.
6 Ndipo mau awa ndikuuzanilero, azikhala pamtima panu;
7 ndipo muziwaphunzitsa mwacangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.
8 Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati cizindikilo, ndipo akhale ngati capamphumi pakati pa maso anu.
9 Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu.
10 Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; midzi yaikuru ndi yokoma, imene simunaimanga;