11 Cenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ace, ndi maweruzo ace, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero lino;
12 kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo;
13 ndipo zitacuruka ng'ombe zanu, ndi nkhosa zanu, zitacurukanso siliva wanu ndi golidi wanu, zitacurukanso zonse muli nazo;
14 mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo;
15 amene anakutsogolerani m'cipululu cacikuru ndi coopsaco, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakuturutsirani madzi m'thanthwe lansangalabwi;
16 amene anakudyetsani m'cipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwa; kuti akucepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akucitireni cokoma potsiriza panu;
17 ndipo munganene m'mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira cuma ici.