2 anthu akuru ndi atalitali, ana a Aanaki, amene muwadziwa, amene munamva mbiri yao, ndi kuti, Adzaima ndani pamaso pa ana a Anaki?
3 Potero mudziwe lero lino, kuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene aoloka pamaso panu ngati moto wonyeketsa; iye adzawaononga, iye adzawagwetsa pamaso panu; potero mudzawapitikitsa, ndi kuwaononga msanga, monga Yehova analankhula ndi inu.
4 Musamanena mumtima mwanu, atawapitikitsa pamaso panu Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Cifukwa ca cilungamo canga Yehova anandilowetsa kudzalandira dziko ili; pakuti Yehova awapitikitsa pamaso panu cifukwa ca zoipa za amitundu awa.
5 Simulowa kulandira dziko lao cifukwa ca cilungamo canu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu cifukwa ca zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo.
6 Potero mudziwe, kuti Yehova Mulungu wanu sakupatsani dziko ili lokoma mulilandire, cifukwa ca cilungamo canu; pakuti inu ndinu mtundu wa aathu opulukira.
7 Kumbukilani, musamaiwala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m'cipululu; kuyambira tsikuli munaturuka m'dziko la Aigupto, kufikira munalowa m'malo muno munapiktsana ndi Yehova.
8 M'Horebe momwe munautsa mkwiyo wa Yehova; ndipo Yehova anakwiya nanu kukuonongani.