1 NDIPO Yehova anaitana Mose, nanena naye ali m'cihema cokomanako iye, nati,
2 Lankhula ndi ana a lsrayeli, nunene nao, Ali yense mwa inu akabwera naco copereka ca kwa Yehova, muzibwera naco copereka canu cikhale ca zoweta, ca ng'ombe, kapena ca nkhosa, kapena ca mbuzi.
3 Copereka cace cikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda cirema; abwere nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.
4 Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwace, imtetezere.
5 Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira pa guwa la nsembe, lokhala pa khoma la cihema cokomanako.