3 Copereka cace cikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda cirema; abwere nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.
4 Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwace, imtetezere.
5 Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira pa guwa la nsembe, lokhala pa khoma la cihema cokomanako.
6 Ndipo asende nsembe yopsereza, ndi kuikadzula ziwalo zace.
7 Ndipo ana a Aroni asonkhe mota pa guwa la nsembe, ndi kukonza nkhuni pamotopo;
8 ndi ana a Aroni, ansembewo, akonze ziwalozo, mutu, ndi mafuta pa nkhuni ziri pa mota wa pa guwa la nsembe;
9 koma atsuke ndi madzi matumbo ace ndi miyendo yace; ndi wansembe atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.